Lyrics

Msamatiponye inu eni ake achuma Musamatiponye miyala Nafenso ndi wanthu Msamatitembelele m'malo motidalitsa Joseph Mkasa akuti musamanyoze amphawi Achuma nanu mudzilemekeza wosawuka Tikamaswa nsabwe musamatiyese otembeleledwa Tilibe zifukwa kapena mangawa ndi Mulungu Mukamatiseka m'makhala ngati mukutidzudzula Mabala a umphawi amene alibe ma dokotala Sitimada nkhawa ife chachikulu nabola moyo Chauta mwina ndiyemwe adziwa kusintha nyego Ukasawuka usatenge chingwe kudzipha nacho Ndikuwuzeni ngati munafika kwa Mayaka Che Bauleni pa sitolo yawo analemba Mukawelenga kuti zabwino zili mtsogolo Mtima m'malo Tafatsani Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo Usalire, nzanga osawuka Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo Tidzalemela ife Tidzachita bwino Tizangangalala, nthawi yathu izafika Ndizolembalemba, nzolembalemba Ndizosayinasayina Zonse zidikira nyengo Anzanu ena anachita mwano posamuka Anamenya anthu, kutukwana mfumu m'mudzi muno Mbewu ku dimba adakapopela poison Kutsilika minda kuti atalime awone mbwadza Anakumba munsewu ndi mulata adawuthyola Kunali chi ngongole ku kalabu anathawitsa Anadula minga kukayiwunjika pa m'jigo Anasiya anthu atawawombanitsa mitu Anayiwala kuti chawuluka chizatela Ntchetche inati mtsogolo moyo m'mbuyo moyo Mtima m'malo Tafatsani Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo Usalire, nzanga osawuka Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo Tidzalemela ife Tidzachita bwino Tizangangalala, nthawi yathu izafika Ndizolembalemba, nzolembalemba Ndizosayinasayina Zonse zidikira nyengo Mtima m'malo Tafatsani Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo Usalire, nzanga wosawuka Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo Tidzalemela ife Tidzachita bwino Tizangangalala, nthawi yathu izafika Ndizolembalemba, nzolembalemba Ndizosayinasayina Zonse zidikira nyengo Mtima m'malo Tafatsani Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo Usalire, nzanga wosawuka Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo Tidzalemela ife Tidzachita bwino Tizangangalala, nthawi yathu izafika Ndizolembalemba, nzolembalemba Ndizosayinasayina Zonse zidikira nyengo Mtima m'malo Tafatsani Timufuse Mulungu zabwino zili mtsogolo Usalire, nzanga wosawuka Tizipempha Mulungu zambwino zili mtsogolo Tidzalemela ife Tidzachita bwino (Tizangangalala, nthawi yathu izafika)
Lyrics powered by www.musixmatch.com
instagramSharePathic_arrow_out